Mtsikana wina yemwe amagwila ntchito ya uphunzitsi pa sukulu ina ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota akulila usiku ndi usana mai ake omubala atamuthetsela banja.
Nkhani-yi ikuti mtsikana-yo atayamba ntchito anaganiza zokwatiwa koma amuna samamufunsila.
Kenaka panamveka mphekesela yoti mai ake anamuchitila mankhwala kuti asakwatiwe ati poganiza kuti zonse zomwe amawachitila mai ake-wo asiya.
Apa mtsikana-yo akuti naye anaganiza zopondaponda ndipo anapeza mtela omwe unakwanitsa kumumasula ku msinga za mai ake-wo.
Ndipo posakhalitsa mtsikana-yo anapeza banja. Awiri-wa akuti anagwilizana kuti adzikhala mnyumba yomwe mtsikana-yo anamanga kwao.
Koma mmalo mokondwa mai wa mtsikana-yo kuti anayamba kupezela zifukwa mwamuna-yo ponena kuti ndi mphawi.
Koma ngakhale mtsikana-yo anayesetsa kuikila kumbuyo mwamuna wake mkutemetsa nkhwangwa pa mwala kuti sasiyana ndi mwamuna-yo naye mai-yo anachita chotheka mpaka kuthetsa banja-lo.
Mtsikana-yo akuti anadandaula kwambiri ndi zomwe mai ake anachita. Koma patangotha miezi yochepa mtsikana-yo akuti anakwatiwanso ndi mkulu wina. Mai wa mtsikana-yo mmalo mokondwa kuti mwamuna wa tsopano-yo yemwe anali wamakobili ake akuti anapitiliza kuvutitsa mwana wake kuti athetse banja-lo.
Mai-yo akuti anayamba kumalalatila mpongozi-yo pa maso ndipo mpongozi-yo atatopa ndi khalidwe-li anathetsa banja-lo. Pakadali pano mtsikana-yo akuti akukhala khuma kamba ka zomwe mai ake amuchita.