Anthu a m’mudzi wina mdera la Mfumu Mabulabo mboma la Mzimba anafa ndi phwete pamene mkulu wina anamenyedwa ndi mwana wachichepere chifukwa chozemba kubweza ngongole.
Nkhaniyi ikuti m’deralo muli mwana wina yemwe amagulitsa mandasi ndipo akuti anthu ambili anamuzolowera pomwe nthawi zina amatha kuwakongoza nkudzatenga ndalamazo tsiku lotsatira.
Patsikulo mkuluyo atamuona mwanayo, anamuitanitsa nkutengamo mandasi anayi pa mtengo wa 2 hundred kwacha. Mwanayo atafunsa za ndalama, anamuyankha kuti akayendayenda abwerenso pamalopo akatenge ndalama yake chifukwa pa nthawiyo anali ndi yosasintha.
Apatu mwanayo anakhulupilira zimenezi kamba koti anamuonetsa 2 thousand kwacha yosasintha. Koma mwanayo anakhumudwa atapitanso kwa mkuluyo kuti akatenge ndalama yakeyo, kumupeza palibe.
Kuyambira tsikulo,mkuluyo wakhala akuzemba ngongoleyo, koma poti amati chozemba chidakumana nchokwawa, patsikulo mkuluyo anangoti gululu ndi mwanayo.
Atamufunsa za ndalamayo anayankha mwa thamo amvekere adzabweza ngongoleyo akadzafuna zomwe sizinasangalatse mwanayo.
Pamenepa mwanayo anayamba kumuvutitsa mkuluyo kuti amupatse ndalama yakeyo koma mkuluyo m’malo mongopereka ndalamyo anamuponyera chibakera mwanayo.
Apatu mwanayo anazinda chibakeracho zomwe zinachititsa kuti mkuluyo agwe yekha ndi chibakeracho. Nthawi yomweyo mwanayo anathamanga kukamukhalira mkuluyo pa msana nkuyamba kumuumbuza.
Anthu omwe amaonelera ndeuyo, anafa ndi phwete maka poganizira momwe mkuluyo anagwera ndi chibakera chake chomwe. Izitu zimachitika, ana ena omwe amachokera ku sukulu akuchemelera nzawoyo ngati muja achitira pa masewero a nkhonya.
Ataona kuti zavuta mkuluyo anangomuluma mwanayo ndipo nthawi yomweyo anadzukao pamsanapo, ndeuyo nkuthera pomwepo.
Pakadali pano mkuluyo walumbira kuti sapereka ngongoleyo ati kamba koti ndalamayo yalowa m’malo mwa chipongwe chomwe mwanayo wachita pomuvivinyiza m’dothi, anthu akuona.