Mkulu wina ku Thondwe mboma la Zomba wapita ku Lilongwe asakufuna, mbili itamveka kuti wapereketsa ndalama yokwana 200 thousand kwacha chifukwa chofuna kulemera.
Nkhaniyi ikuti mkuluyo amachita geni kuyambira kalekale koma akuti zinthu sizimayenda. Ali mwapenda-penda chomwecho, m’deralo munafika munthu wina yemwe amanamiza anthu kuti ali ndi mankhwala wothandiza anthu omwe akufuna kulemera.
Mkuluyo atamva izi, anadololoka mtima mpaka kumufunafuna munthuyo kuti amuthandize pa nkhaniyi. Awiriwa atakumana, anakambirana zofunika kuchita kulemerako kusanadze ndipo anamuuza mkuluyo kuti apereke K2,00 000 yoti akayankhulirane ndi azimu.
Chifukwa chotopa ndi umphawi, mkuluyo anakunkhakunkha ndalamayo nkumuninkha munthuyo pomwe anamutsimikizira kuti sipatha sabata, awona zodabwitsa ku nyumba kwake. Mwa zina munthuyo anauza mkuluyo kuti akapeze chisaka chabwino chomwe amati mudzifikira ndalamazo azimu akangoyankha. Izitu zimachitika pa uwiri wawo moti palibe amadziwa zomwe anthuwa amakambirana.
Koma nkhaniyi inaululika pamene mkuluyo anadikira mpaka sabata ziwiri koma popanda cholowa mu sakamo. Kenaka atayamba kumufufuza munthuyo, anazindikira kuti ndi mbava chifukwa ambili amati sakumudziwa ndi wachilendo m’deralo. Apa mkuluyo anazungulira mutu mpaka kumamusaka munthuyo m’nthumba la buluku. Chifukwa cha manyazi, mkuluyo wangosowa m’deralo pomwe watsanzika achibale ake kuti akupita ku Lilongwe kuti mwina ikamupite mphepo ina.